‎Slessor wapempha Lawi, akuti ndibwino nkhondoyi ikakhale Yama freestyle.

Support our Youtube Channel, Subscribe

‎Pamene oyimba wa Chamba Cha lokolo “Lawi” tsopano wakhazikika pa mfundo yake yopangitsa Mkumano wa mphangala za Hip Hop kuno ku Malawi otchedwa “Battle of the Mcees”, ena mwa oyimba a Hip Hop apempha kuti kumeneko aliense akachite ma freestyle osati kuimba nyimbo zomwe adayimba kalekale. Iwo akuti ikakhale live battle, “bar for bar”


Forex Ikuvuta? Mutha ku order katundu kunja Kwa Dziko lino kudzela pa card la Visa Debit Card pogwilitsa ntchito ndalama za Crypto currencies, dinani kuti muyambe..


‎‎Mfundoyi yabwera ndi m’modzi mwaanthu omwe atumphukaso mu Chamba Cha rap patapita nthawi atakhala chete ‘Slessor’. Munkukamba kwake oyimbayu wanenetsa kuti sizinganveke bwino ngati battle imeneyi ikukachitika pa nyimbo zoti zidatchuka kale ndipo zidatha. Akuti ngati zili chomchi mkwabwino kungoitchula imeneyi kuti ndi Rap show osati battle of the Emcees.

‎Pansipo Pali chidutswa Cha zomwe walemba Slessor kudzela pa tsamba lake la Facebook.

Onani zomwe wa posita Slessor pa Facebook

‎Lawi walongosola kuti dongosolo limeneli likhala likuchitika ku Lilongwe, BICC pa 2 May 2026. Ndipo akuti tsiku limeneli likasiyanitsa akatswiriwa. Ndipo anthu akadziwa okha kuti  akamuna ogona kukhomo kosatseka ndiati komanso omwe amangolubwalubwa ndi atiwo.

‎Ngakhale Slessor walankhulapo motere, ambiri akukamba kuti mkutheka iyeyo angofuna kuphiphilitsa potengela kuti papita nthawi yayitali asakutulutsa nyimbo. Ndipo ngati mwambowu uli ofunika anthuwa kukayimba nyimbo zomwe adayimba kale, iyeyo akasowa nyimbo zosangalatsila anthu oonerela..

‎Nazo mphangala zotsata Hip Hop zati zili ndi chikayiko ngati mwambowu uti ukayende bwino potengela kuti, opangitsayu “Lawi” siokhazikika mu Hip Hop. Lawi saadakane kapena kuvomelezana nazo za nkhaniyi, iye posafuna kuchulukitsa Gaga m’diwa, wangoyankhilapi mkunena kuti “mawu”.

Follow us on Facebook

Share This Article
Leave a Comment