Anthu ambiri ali odabwitsika ndi chiganizo chomwe chipani Cha Malawi Congress Party Chachita. Akulu akulu a Chipanichi kudzela mwa a Simplex Chithyola anenetsa kuti saatenga nawo mbali pochita kafukufuku watsopano, pakusakasaka chomwe chidachititsa ngozi ya Ndege ku Chikangawa. Iwo akuti kafukufukuyi ndi nkhamba kamwa chabe komanso kungoononga ndalama.
Chipani chotsutsa cha Malawi Congress Party MCP, chalengeza kuti sichitenga nawo gawo pa kafukufuku watsopano wokhudza ngozi ya ndege yomwe inagwa ku Chikangawa mchaka cha 2024 yomwe idapha wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino ndi anthu ena asanu ndi awiri.
Mkulu wa dzipani zotsutsa mnyumba ya malamulo Simplex Chithyola Banda ndiye wanena kuti chipani cha MCP sichitenga nawo mbali pa kafukufuku ameneyu chifukwa ndizongofuna kuwononga ndalama chipani cha MCP chidapanga kawiri konse kafukufuku wa ndegeyu kotelo iwo ati wina afune ngakhale asafune iwo salora kukafusidwa mafuso.
Chipani chotsutsachi chalengeza kuti sichitenga nawo gawo pa kafukufuku watsopano wokhudza ngozi ya ndege yomwe inagwa ku Chikangawa mchaka cha 2024 ndikutenga moyo wa Vice President panthawiyi komanso anthu ena 8.

Mkulu wa dzipani zotsutsa mnyumba ya malamulo Simplex Chithyola Banda ndiyenwanena izi mnyumba ya malamulo.
Koma ngakhale zili choncho, Banda sananene tsatanetsatane wa dzifuwa zomwe iwo ngati chipani aganiza zosatenda nawo mbali.
Ngoziyi idachitika munthayi ya ulamuliro wa chipani Cha MCP ndipo ambiri ali ndi ganizo lonena kuti report lakafukufuku ameneyi lomwe lidapelekedwa pa nthawiyo lidasoweka chilungamo. Komanso silidakwanitse kuyankha mafunso omwe anthu alinawo pazokhudza ngoziyi..