Jayz wazizwitsa gulu, ma tickets aku show yake atatha mu 5 minutes

Ma show amenewa akuti akukumbukila kuti patha zaka 30 atatulutsa album yake yomwe yoyamba

Brian Mtimaukanena

Support our Youtube Channel, Subscribe

Highlights

‎Jayz, tsopano waganiza zobwerela pa stage. Mkuluyi wayala ma show awiri mu July ku Yankee Stadium, Bronx, New York City.

Ma show amenewa akuti akukumbukila kuti patha zaka 30 atatulutsa album yake yomwe yoyamba “Reasonable beyond doubt” imeneyi inatuluka mu 1996. Show yake ilipo pa July 10, 2026.

Komanso pa 11 July, 2026 akhala akukumbukila kuti patha zaka 25 chitulutsileni album ya “The Blueprint” yomwe inatuluka mu 2001.

Ma tickets ku ma shows amenewa atha patangotenga ma minutes 5 okha kuchoka pamene anafika pa msika. Zikuonetsa kuti pa Ticketmaster panali anthu oposa 1.6 million (23 March 2026) pa mzere, omwe amafunako atapeza ma tickets oti akapezeka ku ma shows amenewa. Ngakhale izi zili choncho Yankee Stadium imalowa anthu osachepela 70 thousand.

‎‎Kuona chiwelengelo Cha Queue, zasonyeza kuti anthu oposa  816,000 anali pa mzere kudikila ma ticket a tsiku loyamba la show pa 10 July. Koma dongosolo logulitsa ma ticket layambika lero pa 24 pa Ticketmaster.

‎Ma show amenewa akubwera patatha zaka 7, kuchoka pamene Jay anabwera ndi mashow akeake komanso ngati iyeyo headliner.

Mitengo ya ma shows amenewa ikutengela malo omwe munthu wasankha kuti akhale komanso kuti akugulira pati. Ngati mukugula Ticket yotchipitsitsa ndi $201 USD ngati mukugula Kwa madobadoba ndi $383.

Ngati mukugula ticketi ya pakatikati Mtengo ndi $600 USD komanso $838 ngati mukugula Kwa madobadoba.

Ndiponso Mtengo wa malo opezeka kutsogolo pafupi ndi stage uli pa $1,200 kufika pa $1,715 mukagula kwa madobadoba.

‎Ticket ya VIP kapena kuti Luxury Packages

kwaamene akufuna zapamwamba ili pa $3000 USD.

‎Ndipo ma tickets a anthu angapo omwe amatchedwa kuti Luxury Suites: For full-service suites, mitengo yake ili pa $7,000 osapitilira $20,000 pa anthu angapo.

Follow us on Facebook

Share This Article
Leave a Comment