TRIEPHORNIA THOMSON MPINGANJIRA WAPELEKA NDALAMA KWA MTSIKANA OGULITSA KAUNJIKA

Elizabeth Munthali

Support our Youtube Channel, Subscribe

Bungwe la Triephornia Thomson Mpinganjira Foundation lathandiza Monalisa Mandala yemwe amagulitsa zovala za kaunjika ku Area 18, mu mzinda wa Lilongwe ndi K3 million.

Monalisa, yemwe ali ndi zaka 26, anayamba malonda ake mu 2021 atangomaliza maphunziro ake a social work ku DMI University, pogwilitsa ntchito ndalama zokwana k15,300.00 zomwe anagulitsa zovala zake za m’thupi.

Thandizoli ladza pomwe msungwanayu analemba patsamba lake la mchezo la Tiktok kuwonetsa kuthodwa ndi bizinesi yake pomwenso ankatsatsa malonda ndi kulimbikitsa achinyamata kuti asamafooke pa bizinesi.

Mayi Mpinganjira atawona uthengawu, anamulonjeza Monalisa kuti amuthandiza pomuwonjezera mpamba wa bizinesi yake kuti ncholinga choti adzathandizenso ena kutsogoloku.

Atalandira nthandizoli ku Area 18, Monalisa anali wodzidzimutsidwa ponena kuti sanayembekezere kuti angadalitsike motere.

Mmawu ake, nthumwi ya bungweli a Wezi Chiweta anati ndicholinga cha bungweli kusitha miyoyo ya Malawi ncholinga choti adzidzidalira pachuma.

Wolemba ndi Elizabeth Munthali, 265 Ent Mag Tv, ( Mzimba,

Follow us on Facebook

Share This Article
Leave a Comment