General Dr. Paul Valentino Phiri walankhula izi mu mzinda wa Lilongwe pa mwambo wotsegulira msonkhano wamasiku awiri wokhudza nkhani zofalitsa nkhani, malamulo a zisankho ndi ndondomeko.
A phiri Ati kupereka malipoti olakwika pachisankho komanso pambuyo pake, kumatha kudzetsa mikangano pakati pa anthu
Iye anatsindika kufunikira kwa akatswiri ofalitsa nkhani kuti amvetsetse malamulo ndi ndondomeko za chisankho, kuti athe kupereka malipoti mosamala ndi kulimbikitsa mtendere m’dziko.
M’mawu ake, wachiwiri kwa wapampando wa bungwe la Malawi Peace and Unity Commission, Reverend Dr. Zacc Kawalala, anatsindika kuti kutsatira mfundo za makhalidwe abwino sikuyenera kwa atolankhani chabe, koma ndi udindo wa nzika aliyese
Olemba
Eron Manda (Lilongwe)