NGOZI INA YAPHA MUNTHU MMODZI KU NTCHEU

Robert Billy

Support our Youtube Channel, Subscribe

Munthu mmodzi akuganizilidwa kuti wafa pomwe ena asanu ndi mmodzi apita nawo kuchipatala atavulala pa ngozi yomwe yachitika m’mudzi mwa Kampepuza, m’boma la Ntcheu.
Malinga ndi mneneli wa apolisi a ku Ntcheu, Jacob Khembo, ngoziyi yachitika pamene truck yonyamula matumba a simenti inagundana ndi galimoto ina, zomwe zinapangitsa thupi la munthu amene wafa kugwera pansi pa truck yomwe inagwa.

A Khembo ati anthu asanu ndi mmodzi omwe anavulala apita nawo kuchipatala cha m’boma la Ntcheu komwe akulandira chithandizo.
Pakadali pano, anthu akumudziwo akupitiriza kuchotsa thupi la malemuyo pansi pa truckyo pamene apolisi akufufuza chomwe chinayambitsa ngoziyo.

Koma pamene ngozi ngati izi zikuchulukirachulukira tsiku ndi tsiku m’dziko muno, mafunso opanda mayankho akuchuliukirachulukirabe pakati pa a Malawi kuti “Kodi kusatsata malamulo apamsewu kwafika potenga miyoyo chochuluka chomchi bwanji?”,Kodi oyendetsa magalimoto akumvetsa bwanji udindo wawo pothandiza kuchepetsa ngozizi?”,Nanga boma likuchitapo chani pothana ndi ngozi zomwe zikupha anthu pafupifupi tsiku lililonse?
Malinga ndi chiwerengero chomwe chinatulutsidwa ndi nthambi ya polisi, ngozi zambiri zimachitika chifukwa cha liwiro lochuluka, kulephera kutsatira zizindikiro za pamsewu, komanso kusagwiritsa ntchito bwino magalimoto.
Ngati malamulo apamsewu sangatsatidwe mosamalitsa, ngozi monga izi ya zikhoza kupitirirabe kutenga miyoyo ya anthu ochuluka kulichete.

Follow us on Facebook

Share This Article
Leave a Comment