Nkulu wa asilikali a nkhondo dziko muno (MDF) wapempha atolankhani m’dziko muno kuti athandize anthu kumvetsetsa bwino za zisankho zomwe zikuyembekezeka kuchitika chaka chino pa 16 September.

Enron Manda

Support our Youtube Channel, Subscribe

General Dr. Paul Valentino Phiri walankhula izi mu mzinda wa Lilongwe pa mwambo wotsegulira msonkhano wamasiku awiri wokhudza nkhani zofalitsa nkhani, malamulo a zisankho ndi ndondomeko.

A phiri Ati kupereka malipoti olakwika pachisankho komanso pambuyo pake, kumatha kudzetsa mikangano pakati pa anthu

Iye anatsindika kufunikira kwa akatswiri ofalitsa nkhani kuti amvetsetse malamulo ndi ndondomeko za chisankho, kuti athe kupereka malipoti mosamala ndi kulimbikitsa mtendere m’dziko.

M’mawu ake, wachiwiri kwa wapampando wa bungwe la Malawi Peace and Unity Commission, Reverend Dr. Zacc Kawalala, anatsindika kuti kutsatira mfundo za makhalidwe abwino sikuyenera kwa atolankhani chabe, koma ndi udindo wa nzika aliyese

Olemba
Eron Manda (Lilongwe)

Follow us on Facebook

Share This Article
Leave a Comment